Skip to content
Baibulo lidalembedwa chifukwa chiyani? episode artwork

Mar 7, 2021 32 min

Baibulo lidalembedwa chifukwa chiyani?

from Chuma mzikho zadothi Hosted by John Joseph Matandika

Ndiye ndi mawu amene akupezeka pa Genesis 1:1 china chilichonse m’moyo chikupatsidwa maonekedwe ake, cholinga chake komanso tanthauzo lake. Ndi chinthu chofunikila komanso kudzichepetsa kuzindikila kuti nkhani ya Baibulo siyidayambe ndi ife. Imayamba ndi Mulungu. Ndi chinthu chofunikila kwambiri kuzindikila kuti pamene nkhani ya masamba a Baibulo ikutambasulidwa ndi nkhani ya Mulungu. Iye wayima pakatipati pa zochitika zonse. Iye ali ndi magawo ofunikila. China chilichonse chikudalira Iye. Nkhaniyo ikuyenda monga mwa chifunilo chake komanso dongosolo lake. Zonse ndi za Iye, zochokela kwa Iye, kudzera mwa Iye, komanso zokhudzana ndi Iye. Ndiye pamenepa titha kupezapo yankho pa funso lathu: ndi chifukwa chiyani Baibulo lidalembedwa? Ndiye mwachidule, Baibulo lidalembedwa kuti lionetsele ulemelero wa Mulungu. Pa Habakuku 2:14 timawelenga kuti “Pakuti dziko lapansi lidzadzazidwa ndi chidziwitso cha ulemelero wa Yehova, monga momwe madzi amadzazira nyanja.” Cholinga chachikulu cha Mulungu polenga komanso kuombola dziko ndi ulemelero wake. Nkhani ya Mulungu cholinga chake ndi kubweletsa ulemelero kwa Mulungu. Tikakumbukila kuti ulemelero wa Mulungu ndiye cholinga cha nkhani ya chiombolo, titha kulingalira zoyenela pa moyo wathu, pa ntchito yathu, pa kudzipeleka kwathu, komanso pa zimene tikwanilitsa.

Episode details come from the podcast's RSS feed.

Embed this episode

Ready to play

Baibulo lidalembedwa chifukwa chiyani?

0:00 32:28

No transcript yet.

Requests help us decide what to transcribe next.

Frequently asked questions

How long is this episode of Chuma mzikho zadothi?

This episode is 32 minutes long.

When was this Chuma mzikho zadothi episode published?

This episode was published on March 7, 2021.

Can I download this Chuma mzikho zadothi episode?

Yes. Use the download control on the episode player to save the publisher-provided media file.