Skip to content
Kodi mpingo umagwila ntchito motani? episode artwork

May 31, 2021 28 min

Kodi mpingo umagwila ntchito motani?

from Chuma mzikho zadothi Hosted by John Joseph Matandika

1 Akorinto 12:12-26 Thupi Limodzi Ziwalo Zambiri 12Thupi ndi limodzi, ngakhale kuti lapangidwa ndi ziwalo zambiri. Ndipo ngakhale ziwalo zake zonse ndi zambiri, zimapanga thupi limodzi. Momwemonso ndi mmene alili Khristu. 13Pakuti tonse tinabatizidwa ndi Mzimu mmodzi mʼthupi limodzi. Myuda kapena Mgriki, kapolo kapena mfulu tonse tinapatsidwa kuti timwe Mzimu mmodzi yemweyo. 14Tsopano thupi silinapangidwe ndi chiwalo chimodzi koma ndi ziwalo zambiri. 15Ngati phazi litanena kuti, “Pakuti sindine dzanja, sindine chiwalo cha thupi.” Chifukwa chimenechi sichingachititse phazi kuti lisakhale chiwalo cha thupi. 16Ndipo ngati khutu litanena kuti, “Pakuti sindine diso, sindine chiwalo cha thupi.” Chifukwa chimenechi sichingachititse khutu kuti lisakhale chiwalo cha thupi. 17Kodi thupi lonse likanakhala diso, tikanamamva bwanji? Nanga thupi lonse likanakhala khutu, tikanamanunkhiza bwanji? 18Koma zoona nʼzakuti, Mulungu anayika ziwalo mʼthupi, chilichonse monga momwe Iye anafunira. 19Nanga zonse zikanakhala chiwalo chimodzi, ndiye thupi likanakhala lotani? 20Mmene zililimu, pali ziwalo zambiri koma thupi ndi limodzi lokha. 21Diso silingawuze dzanja kuti, “Iwe sindikukufuna!” Ndipo mutu sungawuze phazi kuti “Iwe sindikukufuna!” 22Mʼmalo mwake, ziwalo zathupi zimene zimaoneka ngati zofowoka ndizo zili zofunikira kwambiri, 23ndipo ziwalo zathupi zimene timaziyesa zopanda ulemu, ndizo timazilemekeza kwambiri. Ndipo ziwalo zosaoneka bwino ndizo zimalandira ulemu wapadera. 24Koma ziwalo zooneka bwino, nʼkosafunika kuti tizisamalire mwapadera. Mulungu polumikiza ziwalo zathupi, anapereka ulemu wopambana kwa ziwalo zimene zimafunadi ulemuwo 25kuti pasakhale kugawikana mʼthupi koma kuti ziwalo zonse zisamalirane. 26Ngati chiwalo chimodzi chikumva kuwawa, ziwalo zonse zimamvanso kuwawa. Ngati chiwalo chimodzi chilandira ulemu, ziwalo zonse zimakondwera nawo.

Episode details come from the podcast's RSS feed.

Embed this episode

Ready to play

Kodi mpingo umagwila ntchito motani?

0:00 28:23

No transcript yet.

Requests help us decide what to transcribe next.

Frequently asked questions

How long is this episode of Chuma mzikho zadothi?

This episode is 28 minutes long.

When was this Chuma mzikho zadothi episode published?

This episode was published on May 31, 2021.

Can I download this Chuma mzikho zadothi episode?

Yes. Use the download control on the episode player to save the publisher-provided media file.