Skip to content
Kubadwa kwa Yesu episode artwork

Mar 8, 2022 31 min

Kubadwa kwa Yesu

from Chuma mzikho zadothi Hosted by John Joseph Matandika

Makolo a Yesu Khristu Monga mwa Thupi 1Buku lofotokoza za mʼbado wa Yesu Khristu mwana wa Davide, mwana wa Abrahamu: 2Abrahamu anabereka Isake, Isake anabereka Yakobo, Yakobo anabereka Yuda ndi abale ake. 3Yuda anabereka Perezi ndi Zara, amene amayi awo anali Tamara. Perezi anabereka Hezironi, Hezironi anabereka Aramu. 4Aramu anabereka Aminadabu, Aminadabu anabereka Naasoni, Naasoni anabereka Salimoni. 5Salimoni anabereka Bowazi amene amayi ake anali Rahabe, Bowazi anabereka Obedi amene amayi ake anali Rute, Obedi anabereka Yese. 6Yese anabereka Mfumu Davide. Ndipo Davide anabereka Solomoni, amene amayi ake anali mkazi wa Uriya. 7Solomoni anabereka Rehabiamu, Rehabiamu anabereka Abiya, Abiya anabereka Asa, 8Asa anabereka Yehosafati, Yehosafati anabereka Yoramu, Yoramu anabereka Uziya. 9Uziya anabereka Yotamu, Yotamu anabereka Ahazi, Ahazi anabereka Hezekiya. 10Hezekiya anabereka Manase, Manase anabereka Amoni, Amoni anabereka Yosiya. 11Yosiya anali atabala Yekoniya ndi abale ake pamene Ayuda anatengedwa ukapolo kupita ku Babuloni. 12Ali ku ukapolo ku Babuloni, Yekoniya anabereka Salatieli, Salatieli anabereka Zerubabeli. 13Zerubabeli anabereka Abiudi, Abiudi anabereka Eliakimu, Eliakimu anabereka Azoro. 14Azoro anabereka Zadoki, Zadoki anabereka Akimu, Akimu anabereka Eliudi. 15Eliudi anabereka Eliezara, Eliezara anabereka Matani, Matani anabereka Yakobo. 16Yakobo anabereka Yosefe, mwamuna wa Mariya. Mariyayu ndiye anabereka Yesu wotchedwa Khristu. 17Kuyambira pa Abrahamu mpaka pa Davide, pali mibado khumi ndi inayi. Ndipo kuyambira pa Davide mpaka pamene Ayuda anatengedwa kupita ku ukapolo ku Babuloni, pali mibado khumi ndi inayi. Ndiponso kuyambira nthawi ya ukapolo ku Babuloni mpaka pamene Khristu anabadwa, palinso mibado khumi ndi inayi.

Episode details come from the podcast's RSS feed.

Embed this episode

Ready to play

Kubadwa kwa Yesu

0:00 31:20

No transcript yet.

Requests help us decide what to transcribe next.

Frequently asked questions

How long is this episode of Chuma mzikho zadothi?

This episode is 31 minutes long.

When was this Chuma mzikho zadothi episode published?

This episode was published on March 8, 2022.

Can I download this Chuma mzikho zadothi episode?

Yes. Use the download control on the episode player to save the publisher-provided media file.