EPISODE · Apr 13, 2023 · 26 MIN
Kulungamitsidwa Mutu 2
from Chuma mzikho zadothi · host John Joseph Matandika
Monga kwalembedwa, palibe m’modzi wolungama, inde palibe m’modzi; Palibe m’modzi wakudziwitsa, palibe m’modzi wakufunafuna Mulungu; Onsewa apatuka njira, wonsewa pamodzi akhala wopanda phindu; palibe m’modzi wochita zabwino, inde, palibe m’modzi ndithu. M’mero mwawo muli manda apululu; Ndi lilime lawo amanyenga; ululu wa njoka uli pansi pa milomo yawo; M’kamwa mwawo mudzala ndi zotemberera ndi zowawa; Miyendo yawo ichita liwiro kukhetsa mwazi; Kusakaza ndi kusawuka kuli m’njira zawo; Ndipo njira ya mtendere sadayidziwa; Kumuopa Mulungu kulibe pamaso pawo. Ndipo tidziwa kuti zinthu zili zonse chizinena chilamulo zichiyankhulira iwo ali pansi pa chilamulo; kuti pakamwa ponse patsekedwe, ndi dziko lonse lapansi likatsutsidwe pamaso pa Mulungu. Chifukwa chake pamaso pake palibe munthu adzayesedwa wolungama ndi ntchito za lamulo; pakuti uchimo udziwika ndi lamulo. (Rom 3:10-20)
Embed this episode
Ready to play
Kulungamitsidwa Mutu 2
No transcript for this episode yet
Similar Episodes
No similar episodes found.
Similar Podcasts
No similar podcasts found.