Skip to content
Lamulo Lachinayi episode artwork

EPISODE · Mar 8, 2022 · 25 MIN

Lamulo Lachinayi

from Chuma mzikho zadothi · host John Joseph Matandika

Malamulo Khumi 1Ndipo Mulungu anayankhula mawu onse awa nati: 2“Ine ndine Yehova Mulungu wako amene ndinakutulutsa ku Igupto, mʼdziko la ukapolo. 3“Usakhale ndi milungu ina koma Ine ndekha.” 4“Usadzipangire chofanizira chinthu chilichonse chakumwamba kapena cha pa dziko lapansi kapena cha mʼmadzi a pansi pa dziko. 5Usazigwadire kapena kuzipembedza, pakuti Ine Yehova Mulungu wako, ndine Mulungu wansanje, wolanga ana chifukwa cha tchimo la makolo awo mpaka mʼbado wachitatu ndi wachinayi wa iwo amene amadana nane. 6Koma ndimaonetsa chikondi chosasinthika ku mibado miyandamiyanda ya anthu amene amandikonda, ndi kusunga malamulo anga. 7“Usagwiritse ntchito molakwika dzina la Yehova Mulungu wako, pakuti Yehova adzamutenga kukhala wochimwa aliyense amene akugwiritsa ntchito dzina lakelo molakwika. 8“Uzisunga tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika. 9Uzigwira ntchito zako zonse masiku asanu ndi limodzi. 10Koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndi Sabata, tsiku loperekedwa kwa Yehova Mulungu wako. Tsiku limeneli musagwire ntchito iliyonse, inuyo kapena mwana wanu wamwamuna kapena mwana wanu wamkazi, wantchito wanu wamwamuna kapena mdzakazi wanu, ziweto zanu kapena mlendo amene akukhala mʼmudzi mwanu. 11Pakuti Yehova anapanga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zimene zili mʼmenemo mʼmasiku asanu ndi limodzi. Iye anapuma pa tsiku lachisanu ndi chiwiri. Kotero Yehova anadalitsa tsiku la Sabata kuti likhale loyera. 12“Lemekeza abambo ako ndi amayi ako kuti ukhale ndi moyo wautali mʼdziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa. 13“Usaphe. 14“Usachite chigololo. 15“Usabe. 16“Usapereke umboni womunamizira mnzako. 17“Usasirire nyumba ya mnzako. Usasirire mkazi wa mnzako kapena wantchito wake wamwamuna kapena mdzakazi wake, ngʼombe yake kapena bulu wake, kapena chilichonse cha mnzako.” 18Pamene anthu ankamva mabingu ndi kuona ziphaliwali ndi kumvanso lipenga ndi kuona utsi umene umafuka mʼphiri, ananjenjemera ndi mantha. Ndipo iwo anayima patali. 19Ndipo anati kwa Mose, “Iwe utiyankhule ndipo tidzamvera. Koma usalole kuti Mulungu atiyankhule, tingafe.” 20Koma Mose anati kwa anthuwo, “Musachite mantha. Mulungu wabwera kudzakuyesani kuti mukhale ndi mtima woopa Mulungu kuti musamuchimwire.” 21Anthu aja anayima patali koma Mose anayandikira mtambo wakuda kumene kunali Mulungu.

Episode metadata supplied by the publisher feed · Published Mar 8, 2022

Embed this episode

Ready to play

Lamulo Lachinayi

0:00 25:10

No transcript for this episode yet

We transcribe on demand. Request one and we'll notify you when it's ready — usually under 10 minutes.

No similar episodes found.

No similar podcasts found.

Frequently Asked Questions

How long is this episode of Chuma mzikho zadothi?

This episode is 25 minutes long.

When was this Chuma mzikho zadothi episode published?

This episode was published on March 8, 2022.

Can I download this Chuma mzikho zadothi episode?

Yes. Use the download control on the episode player to save the publisher-provided media file.
URL copied to clipboard!